Deuteronomy 23:25 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mukayenda m'njira yodzera m'munda watirigu, mungathe kudyako ngala za tirigu mobudula ndi manja, koma musadule tirigu ndi chikwakwa m'munda mwa mnzanuyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mukalowa m'tirigu wosasenga wa mnansi wanu, mubudule ngala ndi dzanja lanu, koma musasengako ndi chisenga tirigu wachilili wa mnansi wanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mukalowa mʼmunda wa tirigu wa mʼbale wanu, mukhoza kutengako ngala mʼmanja mwanu, koma osasenga tirigu ndi chikwakwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mukalowa m'tirigu wosasenga wa mnansi wanu, mubudule ngala ndi dzanja lanu, koma musasengako ndi zenga tirigu waciriri wa mnansi wanu.