Deuteronomy 23:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iwoŵa sadakupatseniko chakudya kapena madzi pa ulendo wanu uja wochoka ku Ejipito. Ndipo adalemba ntchito Balamu, mwana wa Beori, wa m'mudzi mwa Petori ku Mesopotamiya, kuti akutemberereni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
popeza sanakumana nanu ndi mkate ndi madzi m'njira muja munatuluka m'Ejipito; popezanso anakulembererani Balamu mwana wa Beori wa ku Petori wa Mesopotamiya, kuti akutemberereni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti iwowa sanabwere kudzakulonjerani ndi chakudya kapena madzi pamene mumadutsa pochokera ku Igupto, mʼmalo mwake anakalemba ganyu Balaamu mwana wa Beori wochokera ku Petori ku Mesopotamiya kuti akutemberereni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
popeza sanakukumikani ndi mkate ndi madzi m'njira muja munaturuka m'Aigupto; popezanso anakulembererani Balamu mwana wa Beori wa ku Petori wa Mesapotamiya, kuti akutemberereni.