Deuteronomy 23:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Chauta, Mulungu wanu, sadamumvere Balamuyo. Matembererowo adaŵasandutsa madalitso pa inu, popeza kuti adakukondani inu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova Mulungu wanu sanafune kumvera Balamu; koma Yehova Mulungu wanu anakusandulizirani tembererolo likhale mdalitso, popeza Yehova Mulungu wanu anakukondani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Komabe Yehova Mulungu wanu sanamvere Balaamu koma anatembenuza temberero kukhala dalitso kwa inu chifukwa Yehova Mulungu wanu amakukondani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova Mulungu wanu sanafuna kumvera Balamu; koma Yehova Mulungu wanu anakusandulizirani tembererolo likhale mdalitso, popeza Yehova Mulungu wanu anakukondani.