Deuteronomy 23:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Musaŵanyoze Aedomu. Amene aja ndi abale anu. Musaŵanyoze Aejipito, popeza kuti kale mudaakhala m'dziko mwao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Musamanyansidwa naye Mwedomu, popeza ndiye mbale wanu; musamanyansidwa naye Mwejipito, popeza munali alendo m'dziko lake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Musapeputse Mwedomu pakuti ndi mʼbale wanu ndithu. Musapeputse Mwigupto chifukwa munali alendo mʼdziko lake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Musamanyansidwa naye M-edomu, popeza ndiye mbale wanu; musamanyansidwa naye M-aigupto, popeza munali alendo m'dziko lace.