Deuteronomy 24:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tiyese kuti munthu wakwatira mkazi, pambuyo pake nkunena kuti mkaziyo sakumfuna, chifukwa choti wampeza cholakwa. Alembe kalata yachisudzulo, ndi kumpatsa mkaziyo pamanja, namchotsa pakhomo pake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Munthu akatenga mkazi akhale wake, kudzali, ngati sapeza ufulu pamaso pake, popeza anapeza mwa iye kanthu kosayenera, amlembere kalata wa chilekanitso, ndi kumpereka uyu m'dzanja lake, ndi kumtulutsa m'nyumba mwake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati mwamuna wakwatira mkazi amene sakukondwera naye chifukwa wapeza vuto pa mkaziyo, namulembera mkaziyo kalata ya chisudzulo, namupatsa ndi kumutulutsa mʼnyumba mwake,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Munthu akatenga mkazi akhale wace, kudzali, ngati sapeza ufulu pamaso pace, popeza anapeza mwa iye kanthu kosayenera, amlembere kalata wa cilekanitso, ndi kumpereka uyu m'dzanja lace, ndi kumturutsa m'nyumba mwace.