Deuteronomy 24:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chibwezeni dzuŵa lisanaloŵe, kuti iye afunde usiku. Apo adzakuthokozani, ndipo Chauta, Mulungu wanu, adzakondwera nanu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
polowa dzuwa mumbwezeretu chikolecho, kuti agone m'chovala chake, ndi kukudalitsani; ndipo kudzakukhalirani chilungamo pamaso pa Yehova Mulungu wanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pomalowa dzuwa ukhale utamubwezera mkanjo wakewo kuti akafunde. Pamenepo adzakuthokoza, ndipo amenewa adzawerengedwa ngati machitidwe olungama kwa iweyo pamaso pa Yehova Mulungu wako.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
polowa dzuwa mumbwezeretu cikoleco, kuti agone m'cobvala cace, ndi kukudalitsani; ndipo kudzakukhalirani cilungamo pamaso pa Yehova Mulungu wanu.