Deuteronomy 24:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Wantchito wolembedwa amene ali mmphaŵi ndi wosoŵa, musamamdyerera, ngakhale akhale mnansi wanu kapena mlendo wokhala mumzinda mwanu m'dziko lanulo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Musamasautsa wolembedwa ntchito, wakukhala waumphawi ndi wosauka, wa abale anu kapena wa alendo ali m'dziko mwanu, m'midzi mwanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Osamapezera mwayi pa anthu aganyu osauka ndi aumphawi, kaya ndi Mwisraeli kapena mlendo wokhala mu umodzi mwa mizinda yanu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Musamasautsa wolembedwa nchito, wakukhala waumphawi ndi wosauka, wa abale anu kapena wa alendo ali m'dziko mwanu, m'midzi mwanu.