Deuteronomy 24:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku lililonse dzuŵa lisanaloŵe, muzimlipira malipiro a tsikulo. Ndalamazo akuzisoŵa iyeyo ndipo akuŵerengera zomwezo. Mukapanda kumlipira, adzakulirirani kwa Mulungu ndipo mudzatsutsidwa kuti ndinu ochimwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pa tsiku lake muzimpatsa kulipira kwake, lisalowepo dzuwa; pakuti ndiye waumphawi, ndi mtima wake ukhumba uku; kuti angakulirireni kwa Yehova, ndipo kukukhalireni tchimo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mumulipire malipiro ake a tsiku dzuwa lisanalowe chifukwa ndi wosauka ndipo akudalira malipirowo. Kupanda kutero adzakudandaulirani kwa Yehova ndipo mudzapezeka ochimwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pa tsiku lace muzimpatsa kulipira kwace, lisalowepo dzuwa; pakuti ndiye waumphawi, ndi mtima wace ukhumba uku; kuti angakulirireni kwa Yehova, ndipo kukukhaireni cimo.