Deuteronomy 24:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mukamakolola dzinthu m'minda mwanu, zina pang'ono nkuiŵalika, musabwerere kukatenga zoiŵalikazo. Zimenezo muzisiyire alendo okhala nanu, ana amasiye ndi akazi amasiye, ndipo Chauta, Mulungu wanu, adzakudalitsani pa ntchito zanu zonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mutasenga dzinthu zanu m'munda mwanu, ndipo mwaiwala mtolo m'mundamo, musabwererako kuutenga; ukhale wa mlendo, wa mwana wamasiye, ndi wa mkazi wamasiye; kuti Yehova Mulungu wanu akudalitseni m'ntchito zonse za manja anu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mukamakolola mʼmunda mwanu ndipo zokolola zina zikasiyidwa, musamabwerere kukazitola. Muzilekere alendo, ana ndi akazi amasiye, kuti Yehova Mulungu wanu akudalitseni pa zochita zanu zonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mutasenga dzinthuzanu m'munda mwanu, ndipo mwaiwala mtolo m'mundamo, musabwererako kuutenga; ukhale wa mlendo, wa mwana wamasiye, ndi wa mkazi wamasiye; kuti Yehova Mulungu wanu akudalitseni m'nchito zonse za manja anu.