Deuteronomy 24:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
ndipo pambuyo pake winayonso nkunena kuti sakumfuna, angathe kumlemberanso kalata yachisudzulo nkumpatsa. Mkaziyo atachokapo pakhomopo, kapena mwamuna wachiŵiri uja atafa,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo akamuda mwamuna wachiwiriyo, nakamlemberanso kalata wa chilekanitso, ndi kumpereka uyu m'dzanja lake, nakamtulutsa m'nyumba mwake; kapena akamwalira mwamuna wotsirizayo, amene anamtenga akhale mkazi wake;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndipo mwamuna wachiwiriyo nʼkuyipidwa nayenso ndi kumulemberanso kalata ya chisudzulo nʼkumutulutsa mʼnyumba mwake, kapena ngati mwamunayo amwalira,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo akamuda mwamuna waciwiriyo, nakamlemberanso kalata wa cilekanitso, ndi kumpereka uyu m'dzanja lace, nakamturutsa m'nyumba mwace; kapena akamwalira mwamuna wotsirizayo, amene anamtenga akhale mkazi wace;