Deuteronomy 24:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
mwamuna wake woyamba uja sayenera kumkwatiranso, ayenera kumuwona ngati woipitsidwa. Kumkwatiranso nkuchimwa pamaso pa Chauta. Tsono musaloŵemo ndi cholakwa m'dziko limene Chauta, Mulungu wanu, akukupatsanilo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
pamenepo mwamuna woyamba anamchotsayo sangathe kumtenganso akhale mkazi wake, atadetsedwa iye; pakuti ichi ndi chonyansa pamaso pa Yehova; ndipo usamachimwitsa dziko, limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale cholandira chanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
mwamuna wake woyamba uja, amene anamuleka saloledwanso kumukwatira kachiwiri popeza mkaziyo wadetsedwa. Chimenechi ndi chonyansa pamaso pa Yehova. Musalowetse tchimo mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani ngati cholowa chanu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
pamenepo mwamuna woyamba anamcotsayo sangathe kumtenganso akhale mkazi wace, atadetsedwa iye; pakuti ici ndi conyansa pamaso pa Yehova; ndipo usamacimwitsa dziko, limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale colandira canu.