Deuteronomy 24:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munthu akangokwatira kumene, musamlembe m'gulu la ankhondo, kapena kumpatsa ntchito ina iliyonse. Papite chaka chathunthu asanachite zimenezi, kuti choncho athe kukhala kwao ndi kumakondweretsa mkazi wake amene adamkwatirayo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Munthu akatenga mkazi watsopano, asatuluke nayo nkhondo, kapena asamchititse kanthu kalikonse; akhale waufulu kunyumba yake chaka chimodzi, nakondweretse mkazi adamtengayo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mwamuna akangokwatira kumene asamatumizidwe ku nkhondo kapena kupatsidwa ntchito ina iliyonse. Kwa chaka chathunthu akhale ndi ufulu wokhala pa khomo pake kumasangalatsa mkazi wakeyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Munthu akatenga mkazi watsopano, asaturuke nayo nkhondo, kapena asamcititse kanthu kali konse; akhale waufulu ku nyumba yace caka cimodzi, nakondweretse mkazi adamtengayo.