Deuteronomy 24:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mukakongoza munthu kanthu, musamtengere mphero yake yoperera tirigu kuti ikhale pinyolo. Kumlanda chimenechi, ndiye kumchotsera chinthu chomuthandiza pa moyo wake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Munthu asalandire chikole mphero, ngakhale mwanamphero, popeza alandirapo chikole moyo wa munthu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Munthu akakhala nanu ndi ngongole musamutengere mwala wake wa mphero ngati chikole, chifukwa kutero nʼkumutengera moyo kukhala chikole cha ngongole.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Munthu asalandire cikole mphero, ngakhale mwanamphero, popeza alandirapo cikole moyo wamunthu.