Deuteronomy 24:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Aliyense woba Mwisraele mnzake ndi kumsandutsa kapolo kapena kumgulitsa ngati kapolo, aphedwe ndithu. Motero mudzachotsa choipa chimenechi pakati pa inu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Akampeza munthu waba mbale wake wina wa ana a Israele, namuyesa kapolo, kapena wamgulitsa, afe wakubayo; potero muzichotsa choipacho pakati panu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati munthu agwidwa akuba mʼbale wake wa Chiisraeli namamuzunza ngati kapolo kapena kumugulitsa, wogulitsa mnzakeyo ayenera kuphedwa. Muyenera kuchotsa choyipa pakati panu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Akampeza munthu waba mbale wace wina wa ana a Israyeli, namuyesa kapolo, kapena wamgulitsa, afe wakubayo; potero muzicotsa coipaco pakati panu.