Deuteronomy 24:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kunena za nthenda ya khate, muwone ndithu kuti mukutsatadi malangizo onse amene ndapatsa ansembe Achilevi, ana a Levi, kuti akuuzeni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chenjerani nayo nthenda yakhate, kusamaliratu, ndi kuchita monga mwa zonse akuphunzitsani ansembe Alevi; monga ndinalamulira iwo, momwemo muzisamalira kuchita.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakagwa matenda a khate, samalitsani kuchita zonse zimene ansembe, amene ndi Alevi, anakulangizani. Mutsatire mosamalitsa zimene ndinawalamula.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cenjerani nayo nthenda yakhate, kusamaliratu, ndi kucita monga mwa zonse akuphunzitsani ansembe Alevi; monga ndinalamulira iwo, momwemo muzisamalira kucita.