Deuteronomy 25:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tiyese kuti anthu aŵiri akangana. Tsono atapita ku bwalo lamilandu, aweruzi nkugamula kuti uyu sadalakwe koma wolakwa ndi winayu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakakhala ndeu pakati pa anthu, nakapita kukaweruzidwa iwowa, nakaweruza mlandu wao oweruza; azimasula wolungama, namange woipa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu akasemphana mawu, ayenera kupita ku bwalo la milandu ndipo woweruza adzaweruza mlanduwo. Adzamasula wosalakwa nalanga wolakwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakakhala ndeu pakati pa anthu, nakapita kukaweruzidwa iwowa, nakaweruza mlandu wao oweruza; azimasula wolungama, namange woipa.