Deuteronomy 25:15 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Miyeso ikhale miyeso yeniyeni yabwino, kuti mukakhale nthaŵi yaitali m'dziko limene Chauta, Mulungu wanu, akukupatsani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Muzikhala nao mwala wa muyeso wofikira ndi woyenera; mukhale nao muyeso wa efa wofikira ndi woyenera; kuti masiku anu achuluke m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Muyenera kukhala ndi miyeso ndi milingo yoyenera ndi yosanyenga kuti mukhalitse mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Muzikhala nao mwala wa muyeso wofikira ndi woyenera; mukhale nao muyeso wa efa wofikira ndi woyenera; kuti masiku anu acuruke m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani.