Deuteronomy 25:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Analibe mantha ndi Mulungu. Motero adakuthirani nkhondo pa njira, pamene mudaali mutatheratu nkutopa. Paja adaŵapheratu anzanu onse amene ankachedwa ndi kuyenda m'mbuyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kuti anakomana ndi inu panjira, nakantha onse ofooka akutsala m'mbuyo mwanu, pakulema ndi kutopa inu; ndipo sanaope Mulungu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene munali otopa ndi ofowoka, iwo anakumana nanu pa ulendo wanu ndi kukantha onse otsalira mʼmbuyo ndipo iwo sanaope Mulungu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kuti anakomana ndi inu panjira, nakantha onse ofok a akutsala m'mbuyo mwanu, pakulema ndi kutopa inu; ndipo sanaopa Mulungu,