Deuteronomy 25:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero tsono, Chauta, Mulungu wanu, akadzakupatsani dziko kuti likhale choloŵa chanu, nadzakulanditsani m'manja mwa adani anu onse okuzungulirani, kasamaleni kuti mukaphe Aamaleke onse, kuti munthu asadzaŵakumbukenso mpang'ono pomwe. Musaiŵale zimenezi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kudzali, pamene Yehova Mulungu wanu atakupumulitsirani adani anu onse ozungulira, m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale cholowa chanuchanu, kuti muzifafaniza chikumbutso cha Amaleke pansi pa thambo; musamaiwala.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene Yehova Mulungu wanu akupumulitsani kwa adani onse okuzungulirani mʼdziko limene akupatsani inu ngati cholowa chanu, mudzawafafanize Aamaleki, asadzawakumbukirenso pa dziko lapansi. Musadzayiwale chimenechi!
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kudzali, pamene Yehova Mulungu wanu atakupumulitsirani adani anu onse ozungulira, m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale colowa canu canu, kuti muzifafaniza cikumbutso ca Amaleki pansi pa thambo; musamaiwala.