Deuteronomy 25:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ngati wolakwayo ayenera kukwapulidwa, muweruziyo amlamule kuti agone pansi ndipo akwapulidwe mikwapulo yolingana ndi kulakwa kwake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kudzali, wochita choipa akayenera amkwapule, woweruza amgonetse kuti amkwapule pamaso pake, amwerengere zofikira choipa chake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Munthu akapezeka wolakwa ayenera kukwapulidwa, woweruza amugoneke pansi wolakwayo ndipo akwapulidwe pamaso pake zikoti zochuluka molingana ndi mlandu wake,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kudzali, wocita coipa akayenera amkwapule, woweruza amgonetse kuti amkwapule pamaso pace, amwerengere zofikira coipa cace.