Deuteronomy 25:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Angathe kumkwapula mpaka mikwapulo makumi anai, koma osapitirira pamenepo. Zikapitirira pamenepo, ndiye kuti zidzamchititsa manyazi mbale wanuyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Amkwapule kufikira makumi anai, asaonjezepo; pakuti, akaonjezapo ndi kumkwapula mikwapulo yambiri, angapeputse mbale wanu pamaso panu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
koma asamukwapule zikoti zopitirira makumi anayi. Akakwapulidwa kupitirira apo ndiye kuti mʼbale wanuyo anyozeka pamaso panu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Amkwapule kufikira makumi anai, asaonjezepo; pakuti, akaonjezapo ndi kumkwapula mikwapulo yambiri, angapeputse mbale wanu pamaso panu.