Deuteronomy 25:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Abale aŵiri akamakhala pamodzi, ndipo wina nkumwalira, koma osasiya mwana, mkazi wamasiyeyo asakwatiwe ndi munthu wa banja lina. Mbale wake wa malemuyo amtenge, amkwatire ndipo apitirize ntchito ya mbale wake kwa mkazi ameneyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Abale akakhala pamodzi, nafa wina wa iwowa, wopanda mwana wamwamuna, mkazi wa wakufayo asakwatibwe ndi mlendo wakunja; mbale wa mwamuna wake alowane naye, namtenge akhale mkazi wake, namchitire zoyenera mbale wa mwamuna wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati abale akukhala pamodzi ndipo wina mwa iwo akamwalira wosasiya mwana wamwamuna, mkazi wamasiyeyo asakakwatiwe ndi mlendo. Mʼbale wake wa mwamuna wakeyo amukwatire kukwaniritsa chimene akuyenera kuchita kwa mlamu wakeyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Abale akakhala pamodzi, nafa wina wa iwowa, wopanda mwana wamwamuna, mkazi wa wafayo asakwatibwe ndi mlendo wakunja; mbale wa mwamuna wace alowane naye, namtenge akhale mkazi wace, namcitire zoyenera mbale wa mwamuna wace.