Deuteronomy 25:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma ngati mbale wa malemuyo samufuna mkazi wa mbale wakeyo, mkaziyo angathe kupita ku chipata kwa akuluakulu ndi kukadandaula kuti, “mbale wa mwamuna wanga uja sakufuna kuti dzina la mbale wakeyo lipitirire m'dziko la Israele. Akukana kundiloŵa chokolo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ngati mwamunayo safuna kutenga mkazi wa mbale wake, mkazi wa mbale wakeyo azikwera kunka kuchipata, kwa akulu, ndi kuti, Mbale wa mwamuna wanga akana kuutsira mbale wake dzina m'Israele; safuna kundichitira ine zoyenera mbale wa mwamuna.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Komabe, ngati munthu sakufuna kukwatira mkazi wa mʼbale wakeyo, mkaziyo ayenera kupita kwa akuluakulu ku chipata cha mzinda ndi kukanena kuti, “Mʼbale wake wa mwamuna wanga akukana kupitiriza dzina la mʼbale wake mu Israeli. Iye akukana kulowa chokolo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ngati mwamunayo safuna kutenga mkazi wa mbale wace, mkazi wa mbale waceyo azikwera kumka kucipata, kwa akuru, ndi kuti, Mbale wa mwamuna wanga akana kuutsira mbale wace dzina m'Israyeli; safuna kundicitira ine zoyenera mbale wa mwamuna.