Deuteronomy 25:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
mkaziyo apite kwa mlamu wakeyo pamaso pa akuluakulu onsewo, ndipo amuvule nsapato yakumodzi, amthire malovu kumaso ndi kunena kuti, “Zimenezi ndiye zoyenera kumchitikira munthu wokana chokolo cha mbale wake.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
pamenepo mkazi wa mbale wake azimyandikiza pamaso pa akulu, nachotse nsapato yake ku phazi la mwamunayo, ndi kumthira malovu pankhope pake, ndi kumyankha ndi kuti, Atere naye mwamuna wosamanga nyumba ya mbale wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
mkazi wamasiye wa mʼbale wakeyo adzapita kwa iye pamaso pa akuluakuluwo namuvula nsapato imodzi, adzamulavulire kumaso nʼkunena kuti, “Izi ndi zimene amachitira munthu amene safuna kupitiriza mbiri ya banja la mʼbale wake.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
pamenepo mkazi wa mbale wace azimyandikiza pamaso pa akuru, nacotse nsapato yace ku ph zi la mwamunayo, ndi kumthira malobvu pankhope pace, ndi kumyankha ndi kuti, Atere naye mwamuna wosamanga nyumba ya mbale wace.