Deuteronomy 26:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chaka chachitatu chilichonse muzipereka chopereka chachikhumi cha zokolola zanu kwa Alevi, alendo, ana amasiye ndi akazi amasiye, kuti kumizinda kumene amakhala iwoŵa, adzakhale ndi chakudya chokwanira. Mutachita zimenezi,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mutatha kugawa magawo khumi, zobala zanu zonse chaka chachitatu, ndicho chaka chogawa magawo khumi, muzizipereka kwa Mlevi, kwa mlendo, kwa mwana wamasiye, ndi kwa mkazi wamasiye, kuti adye m'midzi mwanu, ndi kukhuta.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mukatha kupatula chakhumi pa zonse zimene mwakolola mʼchaka chachitatu chimene ndi chaka chakhumi, muzichipereka kwa wansembe, mlendo, ana ndi akazi amasiye, kuti pamenepo adye mʼmizinda yanu nakhuta.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mutatha kugawa magawo khumi, zobala zanu zonse caka cacitatu, ndico caka cogawa magawo khumi, muzizipereka kwa Mlevi, kwa mlendo, kwa mwana wamasiye, ndi kwa mkazi wamasiye, kuti adye m'midzi mwanu, ndi kukhuta.