Deuteronomy 26:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
munene kwa Chauta kuti, “Palibe nchimodzi chomwe chopereka chachikhumi chimene chatsalako m'nyumba mwanga. Zonse ndapereka kwa Alevi, alendo, ana amasiye ndi akazi amasiye, monga mudandilamulira. Sindidanyoze kapena kuiŵalapo malamulo anu ndi limodzi lomwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo munene pamaso pa Yehova Mulungu wanu, Ndachotsa zopatulika m'nyumba mwanga, ndi kuzipereka kwa Mlevi, ndi kwa mlendo, ndi kwa mwana wamasiye, ndi kwa mkazi wamasiye, monga mwa lamulo lanu lonse munandilamulira ine; sindinalakwira malamulo anu, kapena kuwaiwala.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka munene kwa Yehova Mulungu wanu kuti “Ndatulutsamo mʼnyumba mwanga gawo lopatulika ndipo ndalipereka kwa Mlevi, mlendo, ana ndi akazi amasiye, monga mwa zonse zimene munalamula. Sindinapatuke pa zimene munalamula kapena kuyiwala ndi chimodzi chomwe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo munene pamaso pa Yehova Mulungu wanu, Ndacotsa zopatulika m'nyumba mwanga, ndi kuzipereka kwa Mlevi, ndi kwa mlendo, ndi kwa mwana wamasiye, ndi kwa mkazi wamasiye, monga mwa lamulo lanu lonse munandilamulira ine; sindinalakwira malamulo anu, kapena kuwaiwala.