Deuteronomy 26:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa za chachikhumi sindidadyepo nchimodzi chomwe pamene ndinkalira maliro. Pamene ndinali woipitsidwa pa zachipembedzo, sindidagwirepo nchimodzi chomwe. Ndipo sindidaperekepo nchimodzi chomwe kuperekera anthu akufa. Inu Chauta, Mulungu wanga, ndakumverani. Zonse zimene mudalamula za chopereka chachikhumi ndachita.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Sindinadyako m'chisoni changa, kapena kuchotsako podetsedwa, kapena kuperekako kwa akufa; ndamvera mau a Yehova Mulungu wanga; ndachita monga mwa zonse munandilamulira ine.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Sindinadye kalikonse ka gawo lopatulika pamene ndimalira maliro kapena kuchotsapo kalikonse ka gawo lopatulika pamene ndinali wodetsedwa, kapena kuperekako nsembe kwa akufa kalikonse ka gawoli. Ine ndamvera Yehova Mulungu wanga, ndachita chilichonse chimene inu munandilamula.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Sindinadyako m'cisoni canga, kapena kucotsako podetsedwa, kapena kuperekako kwa akufa; ndamvera mau a Yehova Mulungu wanga; ndacita monga mwa zonse munandilamulira ine.