Deuteronomy 26:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yang'anani pansi kuchokera kumwambako ku malo anu oyera, ndipo mudalitse anthu anu Aisraele. Mudalitsenso dziko ili lamwanaalirenji limene mwatipatsali, monga momwe mudalonjezera makolo athu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Penyani muli mokhalamo mwanu mopatulika, m'mwamba, ndipo dalitseni anthu anu Israele, ndi nthaka imene munatipatsa, monga munalumbirira makolo athu, dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yangʼanani pa dziko kuchokera kumwamba, ku malo anu wopatulika, ndi kudalitsa anthu anu Aisraeli ndi dziko loyenda mkaka ndi uchi limene mwatipatsa ife monga momwe munalonjezera pa malumbiro anu kwa makolo athu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Penyani muli mokhalamo mwanu mopatulika, m'mwamba, ndipo dalitseni anthu anu Israyeli, ndi nthaka imene munatipatsa, monga munalumbirira makolo athu, dziko moyenda mkaka ndi uci ngati madzi.