Deuteronomy 26:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Lero mwamdziŵa Chauta kuti ndi Mulungu wanu. Mwalonjeza kumvera Iyeyo, kusunga malangizo ndi malamulo ake, ndi kuchita zonse zimene akulamulani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mwalonjezetsa Yehova lero kuti adzakhala Mulungu wanu, ndi kuti mudzayenda m'njira zake, ndi kusunga malemba ake, ndi malamulo ake, ndi maweruzo ake, ndi kumvera mau ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mwanena motsimikiza lero lino kuti Yehova ndiye Mulungu wanu ndi kuti mudzayenda mʼnjira zake, kusunga malangizo, malamulo ndi zonse akukulamulani ndi kutinso mudzamumvera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mwalonjezetsa Yehova lero kuti adzakhala Mulungu wanu, ndi kuti mudzayenda m'njira zace, ndi kusunga malemba ace, ndi malamulo ace, ndi maweruzo ace, ndi kumvera mau ace.