Deuteronomy 26:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero pa matamando, pa mbiri ndi pa ulemerero adzakukwezani kupambana mitundu ina yonse ya anthu imene adailenga, ndipo mudzakhala anthu ake oyera mtima, monga momwe adalonjezera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kuti akukulitseni koposa amitundu onse anawalenga, wolemekezeka, womveka dzina, ndi waulemu; ndi kuti mukhale mtundu wa anthu wopatulikira Yehova Mulungu wanu monga ananena.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye wanenetsa kuti adzakuyikani kukhala oyamikika, otchuka ndi olemekezeka koposa mitundu yonse imene anayilenga. Komanso mudzakhala anthu opatulika a Yehova Mulungu wanu monga momwe analonjezera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kuti akukulitseni koposa amitundu onse anawalenga, wolemekezeka, womveka dzina, ndi waulemu; ndi kuti mukhale mtundu wa anthu wopatulikira Yehova Mulungu wanu monga ananena.