Deuteronomy 26:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
aliyense mwa inu pa zokolola zonse zoyamba zimene adazipeza m'dziko limene Chauta akukupatsanilo, atengeko zina ndi kuziika m'dengu, ndipo apite nazo ku malo amene Chauta, Mulungu wanu, adasankhula kuti anthu azidzapembedzerako.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kuti muzitengako zoyamba za zipatso zonse za nthaka, zakubwera nazo inu zochokera m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani; ndi kuziika mudengu, ndi kupita ku malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha kukhalitsako dzina lake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
mutengeko zina mwa zipatso zoyamba pa zonse zimene mudzakola mʼnthaka ya dziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani ndi kuziyika mʼdengu. Mukatero mupite kumalo kumene Yehova Mulungu wanu adzakhazikitsako dzina lake
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kuti muzitengako zoyamba za zipatso zonse za nthaka, zakubwera nazo inu zocokera m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani; ndi kuziika mumtanga, ndi kupita ku malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha kukhalitsako dzina lace.