Deuteronomy 26:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apite kwa mkulu wa ansembe amene ali pa ntchito nthaŵi imeneyo, ndipo amuuze kuti, “Tsopano ndadziŵadi kuti Chauta, Mulungu wanga, wandiloŵetsa m'dziko limene adalonjeza makolo athu kuti adzatipatsa ife.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mufike kwa wansembe wakukhala m'masiku awa, ndi kunena naye, Ndivomereza lero lino kwa Yehova Mulungu wako, kuti ndalowa m'dziko limene Yehova analumbirira makolo athu, kuti adzatipatsa ili.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndipo mudzamuwuze wansembe amene ali pa ntchito pa nthawiyo kuti, “Ndikunenetsa lero kwa Yehova Mulungu wanu kuti ndabwera ku dziko limene Yehova analumbirira makolo athu kuti adzatipatsa ife.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mufike kwa wansembe wakukhala m'masiku awa, ndi kunena naye, Ndibvomereza lero lino kwa Yehova Mulungu wako, kuti ndalowa m'dziko limene Yehova analumbirira makolo athu, kuti adzatipatsa ili.