Deuteronomy 26:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono pamaso pa Chauta, Mulungu wanu, muzidzanena kuti, “Kholo langa linali Lachiaramu, munthu wongoyendayenda, amene adapita ku Ejipito ndi banja lake nakakhala kumeneko. Popita kumeneko, anthuwo adaali ochepa, koma pambuyo pake adachuluka nasanduka mtundu waukulu ndi wamphamvu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo muyankhe ndi kuti pamaso pa Yehova Mulungu wanu, Kholo langa ndiye Mwaramu wakuti atayike, natsika kunka ku Ejipito, nagoneragonera komweko ali nao anthu pang'ono, nasandukako mtundu waukulu, wamphamvu, ndi wochuluka anthu ake;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo mudzanenetsa pamaso pa Yehova Mulungu wanu kuti, “Abambo anga anali Mwaramu woyendayenda, anapita ku Igupto ndi anthu ochepa nakhala kumeneko. Pambuyo pake anakhala mtundu waukulu, wamphamvu ndi wochuluka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo muyankhe ndi kuti pamaso pa Yehova Mulungu wanu, Kholo langa ndiye M-aramu wakuti atayike, natsika kumka ku Aigupto, nagoneragonera komweko ali nao anthu pang'ono, nasandukako mtundu waukuru, wamphamvu, ndi wocuruka anthu ace;