Deuteronomy 27:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Atembereredwe aliyense wogona ndi mkazi wa bambo wake, chifukwa wavula mkazi wa bambo wake.” Ndipo anthu onse adzayankhe kuti, “Inde, momwemo!”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Wotembereredwa iye wakugona ndi mkazi wa atate wake; popeza wavula atate wake. Ndi anthu onse anene, Amen.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ndi wotembereredwa munthu amene agonana ndi mkazi wa abambo ake pakuti iye sachitira ulemu pogona pa abambo ake.” Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Wotembereredwa iye wakugona ndi mkazi wa atate wace; popeza wabvula atate wace. Ndi anthu onse anene, Amen.