Deuteronomy 27:25 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Atembereredwe onse olandira chiphuphu kuti aphe munthu wosalakwa.” Ndipo anthu onse adzayankhe kuti, “Inde, momwemo!”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Wotembereredwa iye wakulandira chamwazi chakuti akanthe munthu wosachimwa. Ndi anthu onse anene, Amen.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ndi wotembereredwa munthu amene alandira chiphuphu kuti aphe munthu wosalakwa.” Pamenepo anthu onse adzati, “Ameni!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Wotembereredwa iye wakulandira camwazi cakuti akanthe munthu wosacimwa. Ndi anthu onse anene, Amen.