Deuteronomy 27:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mutatero, mudzalembepo mau onse a malamulo ameneŵa, mukakaloŵa m'dziko lamwanaalirenjilo, limene Chauta, Mulungu wa makolo anu, adakulonjezani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo mulemberepo mau onse a chilamulo ichi, mutaoloka; kuti mulowe m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani, dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi, monga Yehova Mulungu wa makolo anu ananena ndi inu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mulembepo mawu onse a malamulo amenewa pamene muwoloka kulowa mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani, dziko loyenda mkaka ndi uchi, monga momwe Yehova Mulungu wa makolo anu anakulonjezerani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo mulemberepo mau onse a cilamulo ici, mutaoloka; kuti mulowe m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani, dziko moyenda mkaka ndi uci ngati madzi, monga Yehova Mulungu wa makolo anu ananena ndi inu.