Deuteronomy 28:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mukamamvera mau a Chauta, Mulungu wanu, ndi kutsata mosamala malamulo onse amene ndikukupatsani leroŵa, Chauta, Mulungu wanu, adzakukwezani kopambana mitundu yonse ya pa dziko lapansi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kudzali, mukadzamvera mau a Yehova Mulungu wanu mwachangu, ndi kusamalira kuchita malamulo ake onse amene ndikuuzani lero, kuti Yehova Mulungu wanu adzakukulitsani koposa amitundu onse a pa dziko lapansi;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngati mumvera Yehova Mulungu wanu ndi kutsatira mosamalitsa malamulo ake onse amene ndikukupatsani lero lino, Yehova Mulungu wanu adzakukwezani pamwamba pa mitundu yonse ya pa dziko lapansi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kudzali, mukadzamvera mau a Yehova Mulungu wanu mwacangu, ndi kusamalira kucita malamulo ace onse amene ndikuuzani lero, kuti Yehova Mulungu wanu adzakukulitsani koposa amitundu onse a pa dziko lapansi;