Deuteronomy 28:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Komatu mukapanda kumvera bwino mau a Chauta, Mulungu wanu, ndi kutsata malamulo ndi malangizo amene ndikukupatsani lero lino, adzakugwerani matemberero aŵa:
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma kudzali, mukapanda kumvera mau a Yehova Mulungu wanu, kusamalira kuchita malamulo ake onse ndi malemba ake amene ndikuuzani lero, kuti matemberero awa onse adzakugwerani ndi kukupezani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma ngati simumvera Yehova Mulungu wanu ndi kusatsata mosamalitsa malamulo ake ndi malangizo ake onse amene ndikukupatsani lero lino, matemberero awa adzabwera pa inu ndikukugonjetsani:
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma kudzali, mukapanda kumvera mau a Yehova Mulungu wanu, kusamalira kucita malamulo ace onse ndi malemba ace amene ndikuuzani lero, kuti matemberero awa onse adzakugwerani ndi kukupezani,