Deuteronomy 28:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mukamachita zoipa ndi kumkana Mulungu, Iye adzakutumizirani matemberero, chisokonezo ndiponso zokuvutani pa ntchito zanu zonse, mpaka mutaonongeka ndi kufa nonsenu pa kamphindi kochepa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yehova adzakutumizirani temberero, chisokonezeko, ndi kudzudzula monsemo mukatulutsa dzanja lanu kuchita kanthu, kufikira mwaonongeka, kufikira mwatayika msanga, chifukwa cha zochita inu zoipa, zimene wandisiya nazo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova adzakutumizirani matemberero, chisokonezo ndi minyozo pa chilichonse chimene mudzachichita mpaka mudzawonongedwa ndi kukhala bwinja mofulumira chifukwa cha zoyipa zimene mwazichita pa kumutaya Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yehova adzakutumizirani temberero, cisokonezeko, ndi kudzudzula monsemo mukaturutsa dzanja lanu kucita kanthu, kufikira mwaonongeka, kufikira mwatayika rosanga, cifukwa ca zocita inu zoipa, zimene wandisiya nazo,