Deuteronomy 28:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adzakukanthani ndi nthenda zopatsana, zotupatupa ndi zamalungo. Adzakutumiziraninso kutentha koopsa ndi chilala ndiponso chinsikwi ndi chinoni zoononga mbeu zanu. Masoka amenewo adzakhala pa inu mpaka kukufetsani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yehova adzakukanthani ndi nthenda yoondetsa ya chifuwa, ndi malungo, ndi chibayo, ndi kutentha thupi, ndi lupanga, chinsikwi ndi chinoni; ndipo zidzakutsatani kufikira mwatayika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova adzakukanthani ndi nthenda yowondetsa, ya malungo ndi ya zotupatupa, ndi kutentha kwakukulu ndi chilala, ndi chinsikwi ndi chiwawu zimene zidzakusautsani mpaka mutawonongeka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yehova adzakukanthani ndi nthenda yoondetsa ya cifuwa, ndi malungo, ndi cibayo, ndi kutentha thupi, ndi lupanga, cinsikwi ndi cinoni; ndipo zidzakutsatani kufikira mwatayika.