Deuteronomy 28:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adzalola kuti adani anu akugonjetseni. Pokalimbana nawo mudzadzera njira imodzi, koma poŵathaŵa mudzapanga zikuŵa zisanu ndi ziŵiri. Ndipo mafumu onse a pa dziko lapansi adzaopsedwa poona zokuchitikiranizo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yehova adzalola adani anu akukantheni; mudzawatulukira njira imodzi, koma mudzawathawa pamaso pao njira zisanu ndi ziwiri, ndipo mudzagwedezeka pakati pa maufumu onse a dziko lapansi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova adzalola kuti adani anu akugonjetseni. Mudzadzera njira imodzi pokalimbana ndi adani anu koma pothawa mudzabalalika mbali zisanu ndi ziwiri. Mudzakhala chinthu chochititsa mantha pakati pa maufumu onse a dziko lapansi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yehova adzalola adani anu akukantheni; mudzawaturukira njira imodzi, koma mudzawathawa pamaso pao njira zisanu ndi ziwiri, ndipo mudzagwedezeka pakati pa maufumu onse a dziko lapansi.