Deuteronomy 28:29 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ngakhale dzuŵa lili nye, muzidzachita kufufuza njira ngati anthu akhungu. Kalikonse kamene mudzachite simudzalemera nako. Kaŵirikaŵiri azidzakupsinjani ndi kumakuberani, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amene adzakuthandizeni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo mudzafufuza usana, monga wakhungu amafufuza mumdima, ndipo simudzapindula nazo njira zanu; koma mudzakhala wopsinjika, nadzakuberani masiku onse, wopanda wina wakukupulumutsani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Masanasana mudzayenda ngati muli mu mdima, kumafufuzira njira ngati wosaona. Mudzakhala olephera pa chilichonse mungachite. Tsiku ndi tsiku mudzaponderezedwa ndi kuberedwa wopanda wokupulumutsani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo mudzafufuza usana, monga wakhungu amafufuza mumdima, ndipo simudzapindula nazo njira zanu; koma mudzakhala wopsinjika, nadzakuberani masiku onse, wopanda wina wakukupulumutsani.