Deuteronomy 28:30 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mudzafunsira mbeta mtsikana, koma ndi wina amene adzakwatirane naye. Kumanga nyumba mudzamanga ndithu, koma simudzagonamo. Munda wamphesa mudzabzala, koma mphesa zake simudzadyako.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mudzapalana ubwenzi ndi mkazi, koma mwamuna wina adzagona naye; mudzamanga nyumba, osakhala m'mwemo; mudzaoka munda wamphesa, osalawa zipatso zake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mudzachita chinkhoswe ndi mkazi, koma wina adzakulandani ndi kumukwatira. Mudzamanga nyumba koma simudzagonamo. Mudzalima munda wamphesa koma simudzadyako zipatso zake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mudzaparana ubwenzi ndi mkazi, koma mwamuna wina adzagona naye; mudzamanga nyumba, osakhala m'mwemo; mudzanka munda wamphesa, osalawa zipatso zace.