Deuteronomy 28:31 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ng'ombe zanu azidzakupherani mukupenya, koma nyama yake simudzadyako. Abulu anu azikaŵalanda mwamphamvu ndi kupita nawo kwina, inu mukupenya, ndipo sadzakubwezerani. Nkhosa zanu adzazipereka kwa adani anu, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amene adzakuthandizeni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Adzapha ng'ombe yanu, pamaso panu, osadyako inu; adzalanda bulu wanu molimbana pamaso panu, osakubwezerani; adzapereka nkhosa zanu kwa adani anu, wopanda wina wakukupulumutsani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngʼombe yanu yamtheno idzaphedwa inu muli pomwepo koma simudzadyako. Bulu wanu adzalandidwa kwa inu mwamakani osabwera nayenso. Nkhosa zanu zidzapatsidwa kwa adani anu, ndipo palibe amene adzazipulumutsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Adzapha ng'ombe yanu pamaso panu, osadyako inu; adzalanda buru wanu molimbana pamaso panu, osakubwezerani; adzapereka nkhosa zanu kwa adani anu, wopanda wina wakukupulumutsani.