Deuteronomy 28:32 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ana anu aamuna ndi aakazi adzatengedwa ukapolo ndi alendo, inu mukupenya. Tsiku ndi tsiku maso anu adzakhala ali psuu kuyang'anira ngati ana anuwo abwere, koma simudzaphulapo kanthu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Adzapereka ana anu aamuna ndi aakazi kwa anthu a mtundu wina, ndipo m'maso mwanu mudzada ndi kupenyerera, powalirira tsiku lonse; koma mulibe mphamvu m'dzanja lanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ana anu aamuna ndi aakazi adzaperekedwa kwa anthu a mitundu ina ndipo inu mudzafika potopa ndi kulefuka nʼkudikirira tsiku ndi tsiku kuti mwina anawo abwerako.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Adzapereka ana anu amuna ndi akazi kwa anthu a mtundu wina, ndipo m'maso mwanu mudzada ndi kupenyerera, powalirira tsiku lonse; koma mulibe mphamvu m'dzanja lanu.