Deuteronomy 28:36 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adzaipirikitsira ku dziko lachilendo mfumu yanu, pamodzi ndi inu nomwe, kumene inuyo ndi makolo anu simudakhaleko nkale lonse. Kumeneko muzikatumikira milungu ina yopanga ndi mitengo ndi miyala.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yehova adzamukitsa inu, ndi mfumu yanu imene mudzadziikira, kwa mtundu wa anthu umene simudziwa, inu kapena makolo anu; ndipo mudzatumikirako milungu ina ya mitengo ndi miyala.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova adzakuthamangitsirani, inu ndi mafumu anu amene muwayika, ku dziko losadziwika kwa inu ndi kwa makolo anu. Kumeneko mudzakapembedza milungu ina, milungu ya mitengo ndi miyala.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yehova adzamukitsa inu, ndi mfumu yanu imene mudzadziikira, kwa mtundu wa anthu umene simudziwa, inu kapena makolo anu; ndipo mudzatumikirako milungu yina ya mitengo ndi miyala.