Deuteronomy 28:49 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adzaitanitsa mtundu wa anthu ochokera ku malekezero a dziko lapansi, kuti adzamenyane nanu. Anthu a mtundu umenewo amene inu simudziŵa chilankhulo chao, adzakuterani ngati mphungu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yehova adzakutengerani mtundu wa anthu wochokera kutali ku malekezero a dziko lapansi, monga iuluka mphungu; mtundu wa anthu amene simunamva malankhulidwe ao;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova adzakutumizirani mtundu wa anthu kuchokera kutali kumapeto kwa dziko lapansi nudzachita ngati mphungu yowulukira pansi, mtundu wa anthu umene chiyankhulo chawo simudzachimva,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yehova adzakutengerani mtundu wa anthu wocokera kutali ku malekezero a dziko lapansi, monga iuluka mphungu; mtundu wa anthu amene simunamva malankhulidwe ao;