Deuteronomy 28:51 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adzakudyerani ng'ombe zanu pamodzi ndi zakumunda zanu zomwe, mpaka mudzafa ndi njala. Sadzakusiyiraniko mpang'ono pomwe tirigu, vinyo, mafuta aolivi, ng'ombe kapena nkhosa, ndipo mudzafadi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo adzadya zipatso za ng'ombe zanu, ndi zipatso za nthaka yanu, kufikira mwaonongeka; osakusiyirani tirigu, vinyo, kapena mafuta, zoswana ng'ombe zanu, zoswana nkhosa zanu, kufikira atakuonongani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo adzagwira ana a ziweto zanu, natenga zokolola za mʼdziko lanu kufikira mutawonongeka. Iwo sadzakusiyirani tirigu, vinyo watsopano kapena mafuta a olivi, kapena mwana wangʼombe aliyense kapena mwana wankhosa mpaka mutasanduka bwinja.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo adzadya zipatso za ng'ombe zanu, ndi zipatso za nthaka yanu, kufikira mwaonongeka; osakusiyirani tirigu, vinyo, kapena mafuta, zoswana ng'ombe zanu, zoswana nkhosa zanu, kufikira atakuonongani.