Deuteronomy 28:53 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi imene adani anu adzazinga mizinda yanu ndi kukusautsani koopsa, mudzasoŵa chakudya kotheratu, kotero kuti muzidzadya ana anu omwe aamuna ndi aakazi, amene Chauta adakupatsani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mudzadya chipatso cha thupi lanu, nyama ya ana anu aamuna ndi aakazi amene Yehova Mulungu wanu anakupatsani; pakukumangirani tsasa ndi kukupsinjani adani anu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chifukwa cha zosautsa zimene mdani wanu adzabweretsa pa nthawi yokuthirani nkhondo, inu mudzadya ana anu, mnofu wa ana anu aamuna ndi aakazi amene Yehova Mulungu wanu wakupatsani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mudzadya cipatso ca thupi lanu, nyama ya ana anu amuna ndi akazi amene Yehova Mulungu wanu anakupatsani; pakukumangirani tsasa ndi kukupsinjani adani anu.