Deuteronomy 28:56 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ngakhale mkazi woleredwa bwino ndi wolobodoka kotero kuti sangayese nkomwe kupondetsa pansi phazi lake, adzamana mwamuna wake wapamtima ndi ana ake onse
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mkazi wololopoka nkhongono ndi wanyonga pakati pa inu, wosayesa kuponda pansi ndi phazi lake popeza ndiye wanyonga, ndi wololopoka nkhongono, diso lake lidzamuipira mwamuna wa pamtima pake, ndi mwana wake wamwamuna ndi wamkazi;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mayi woleza mtima ndi wachifundo kwambiri pakati panu, uja woti sangayerekeze kuponda pansi, adzabisira mwamuna wake amene amamukonda ndi ana ake omwe aamuna ndi aakazi
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mkazi wololopoka nkhongono ndi wanyonga pakati pa inu, wosayesa kuponda pansi ndi phazi lace popeza ndiye wanyonga, ndi wololopoka nkhongono, diso lace lidzamuipira mwamuna wa pamtima pace, ndi mwana wace wamwamuna ndi wamkazi;